-
Mateyu 17:14-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Atafika kufupi ndi gulu la anthu,+ mwamuna wina anamuyandikira ndipo anamugwadira nʼkunena kuti: 15 “Ambuye, muchitire chifundo mwana wanga wamwamuna, chifukwa akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Nthawi zambiri amagwera pamoto ndiponso mʼmadzi.+ 16 Ndinapita naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa.”
-
-
Maliko 9:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Munthu wina amene anali mʼgululo anamuyankha kuti: “Mphunzitsi, ine ndabweretsa mwana wanga wamwamuna kwa inu chifukwa ali ndi mzimu umene umamulepheretsa kulankhula.+ 18 Mzimuwo umati ukamugwira, umamugwetsera pansi. Akatero amachita thovu mʼkamwa komanso kukukuta mano ndipo amafooka. Ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse koma alephera.”
-