-
Maliko 9:19-27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Iye anayankha kuti: “Inu mʼbadwo wopanda chikhulupiriro,+ kodi ndikhala nanube mpaka liti? Ndipitirize kukupirirani mpaka liti? Bwera nayeni kuno.”+ 20 Choncho iwo anapita naye kwa Yesu. Koma mzimuwo utamuona, nthawi yomweyo unachititsa kuti mwanayo aphuphe. Anagwa pansi nʼkumagubudukagubuduka ndipo ankachita thovu kukamwa. 21 Ndiyeno Yesu anafunsa bambo ake kuti: “Izi zakhala zikumuchitikira kwa nthawi yaitali bwanji?” Bambo a mwanayo ananena kuti: “Kuyambira ali wamngʼono 22 ndipo nthawi zambiri umamugwetsera pamoto komanso mʼmadzi kuti umuwononge. Koma ngati mungathe kuchitapo kanthu, tichitireni chifundo nʼkutithandiza.” 23 Yesu anafunsa bambowo kuti: “Mukuti ‘Ngati mungatheʼ? Chilichonsetu nʼchotheka kwa munthu amene ali ndi chikhulupiriro.”+ 24 Nthawi yomweyo bambo a mwanayo anafuula nʼkunena kuti: “Chikhulupiriro ndili nacho! Limbitsani chikhulupiriro changa!”+
25 Tsopano Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kwa iwo, anakalipira mzimu wonyansawo kuti: “Iwe mzimu wolepheretsa munthu kulankhula komanso kumva, ndikukulamula, tuluka ndipo usadzalowenso mwa iye.”+ 26 Mwanayo atafuula ndi kuphupha kwambiri, mzimuwo unatuluka ndipo ankaoneka ngati wafa, moti anthu ambiri ankanena kuti: “Wamwalira!” 27 Koma Yesu anamugwira dzanja nʼkumudzutsa ndipo mwanayo anaimirira.
-