-
Mateyu 18:1-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Pa nthawi imeneyo, ophunzira anabwera pafupi ndi Yesu nʼkumufunsa kuti: “Ndi ndani kwenikweni amene adzakhale wamkulu kwambiri mu Ufumu wakumwamba?”+ 2 Choncho iye anaitana mwana wamngʼono nʼkumuimika pakati pawo. 3 Kenako anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mukapanda kutembenuka*+ nʼkukhala ngati ana aangʼono, simudzalowa mu Ufumu wakumwamba.+ 4 Choncho aliyense amene adzadzichepetse ngati mwana wamngʼonoyu ndi amene adzakhale wamkulu kwambiri mu Ufumu wakumwamba.+ 5 Ndiponso aliyense amene walandira mwana wamngʼono ngati ameneyu mʼdzina langa walandiranso ine.
-
-
Maliko 9:33-37Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Kenako anafika ku Kaperenao. Ndiyeno pamene anali mʼnyumba anawafunsa kuti: “Mʼnjira muja mumakangana chiyani?”+ 34 Iwo anangokhala chete, chifukwa mʼnjira amakangana kuti wamkulu ndi ndani pakati pawo. 35 Choncho anakhala pansi nʼkuitana ophunzira 12 aja nʼkuwauza kuti: “Ngati aliyense akufuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza pa onse ndiponso mtumiki wa onse.”+ 36 Kenako anatenga mwana wamngʼono nʼkumuimika pakati pawo ndipo anamukumbatira nʼkuwauza kuti: 37 “Aliyense amene walandira mwana wamngʼono+ ngati ameneyu mʼdzina langa, walandiranso ine. Ndipo aliyense amene walandira ine, sanalandire ine ndekha, koma walandiranso Mulungu amene anandituma.”+
-