-
1 Timoteyo 6:17-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Ulangize* anthu achuma mʼdzikoli* kuti asakhale odzikweza, ndiponso kuti asamadalire chuma chosadalirika,+ koma azidalira Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse zomwe timasangalala nazo.+ 18 Uwauze kuti azichita zabwino, akhale olemera pa ntchito zabwino, owolowa manja komanso okonzeka kugawira ena+ 19 kuti asunge bwino chuma chochokera kwa Mulungu chomwe ndi maziko abwino a tsogolo+ lawo nʼcholinga choti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.+
-