-
Mateyu 24:45-47Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
45 Kodi ndi ndani kwenikweni amene ndi kapolo wokhulupirika komanso wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyangʼanira antchito ake apakhomo, nʼkumawapatsa chakudya pa nthawi yoyenera?+ 46 Kapolo ameneyo adzakhala wosangalala, ngati mbuye wake pobwera adzamupeze akuchita zimenezo!+ 47 Ndithu ndikukuuzani, adzamuika kuti aziyangʼanira zinthu zake zonse.
-