-
Mateyu 10:34-36Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Musaganize kuti ndinabwera kudzabweretsa mtendere padziko lapansi. Sindinabwere kuti ndidzabweretse mtendere koma lupanga.+ 35 Ndinabwera kudzagawanitsa anthu. Ndinabwera kudzachititsa kuti mwana wamwamuna atsutsane ndi bambo ake, mwana wamkazi atsutsane ndi mayi ake ndiponso kuti mkazi wokwatiwa atsutsane ndi apongozi ake aakazi.+ 36 Kunena zoona, adani a munthu adzakhala a mʼbanja lake lenileni.
-
-
Yohane 7:43Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
43 Choncho gulu la anthulo linagawanika pa nkhani yokhudza iye.
-