26 Elizabeti ali woyembekezera kwa miyezi 6, Mulungu anatumiza mngelo Gabirieli+ kumzinda wina wa ku Galileya, wotchedwa Nazareti. 27 Anamutumiza kwa namwali+ amene mwamuna wina dzina lake Yosefe, wa mʼnyumba ya Davide, anamulonjeza kuti adzamukwatira. Namwali ameneyu dzina lake anali Mariya.+