-
Maliko 11:7-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Anthuwo anabweretsa bulu uja+ kwa Yesu. Kenako anayala malaya awo akunja pabuluyo ndipo iye anakwerapo.+ 8 Komanso anthu ambiri anayala malaya awo akunja mumsewu ndipo ena anadula masamba mʼminda.+ 9 Ndiyeno amene anali patsogolo komanso amene ankabwera mʼmbuyo ankafuula kuti: “Mʼpulumutseni!+ Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova!*+ 10 Wodalitsidwa ndi Ufumu wa atate wathu Davide+ umene ukubwerawo! Mʼpulumutseni kumwambamwambako!”
-