28 Yesu anacheukira azimayiwo nʼkunena kuti: “Inu ana aakazi a Yerusalemu, siyani kundilirira. Koma mudzilirire nokha ndi ana anu.+ 29 Chifukwa masiku akubwera pamene anthu adzanena kuti, ‘Osangalala ndi akazi amene alibe ana, akazi amene sanaberekepo komanso akazi amene sanayamwitsepo!’+