-
1 Akorinto 1:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Koma ife timalalikira za Khristu amene anaphedwa popachikidwa pamtengo wozunzikirapo.* Ayuda amaona kuti zimenezi nʼzokhumudwitsa ndipo anthu a mitundu ina amaona kuti nʼzopusa.+ 24 Ngakhale zili choncho, Ayuda ndi Agiriki amene anaitanidwa amaona kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru za Mulungu.+
-