Mateyu 3:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Mʼmasiku amenewo, Yohane+ Mʼbatizi anapita mʼchipululu cha Yudeya nʼkuyamba kulalikira.+ Mateyu 3:5, 6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Choncho anthu ochokera ku Yerusalemu ndi mʼchigawo chonse cha Yudeya ndiponso ochokera mʼmidzi yonse yapafupi ndi Yorodano ankapita kwa iye.+ 6 Iye ankawabatiza* mumtsinje wa Yorodano+ ndipo anthuwo ankaulula machimo awo poyera. Maliko 6:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Herode ankaopa Yohane chifukwa ankadziwa kuti ndi munthu wolungama komanso woyera,+ choncho ankamuteteza. Atamva zimene ankanena anathedwa nzeru, komabe anapitiriza kumumvetsera mosangalala.
5 Choncho anthu ochokera ku Yerusalemu ndi mʼchigawo chonse cha Yudeya ndiponso ochokera mʼmidzi yonse yapafupi ndi Yorodano ankapita kwa iye.+ 6 Iye ankawabatiza* mumtsinje wa Yorodano+ ndipo anthuwo ankaulula machimo awo poyera.
20 Herode ankaopa Yohane chifukwa ankadziwa kuti ndi munthu wolungama komanso woyera,+ choncho ankamuteteza. Atamva zimene ankanena anathedwa nzeru, komabe anapitiriza kumumvetsera mosangalala.