37 Pilato anamufunsa kuti: “Chabwino, koma kodi ndiwe mfumu?” Yesu anayankha kuti: “Mukunena nokha kuti ndine mfumu.+ Ndinabadwa komanso ndinabwera mʼdziko kuti ndidzachitire umboni choonadi.+ Aliyense amene ali kumbali ya choonadi amamvetsera mawu anga.”