-
Luka 24:39-41Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
39 Onani manja ndi mapazi angawa, mutsimikize kuti ndine ndithu. Ndikhudzeni muone, chifukwa mzimu ulibe mnofu ndi mafupa ngati anga amene mukuwaonawa.” 40 Pamene ankanena zimenezi, anawaonetsa manja ndi mapazi ake. 41 Koma popeza iwo sankakhulupirirabe chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, iye anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?”
-
-
Yohane 20:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Madzulo a tsiku limenelo, limene linali tsiku loyamba la mlungu, ophunzirawo anasonkhana pamodzi. Mʼnyumba imene anasonkhanayo anakhoma zitseko chifukwa ankaopa Ayuda. Koma Yesu analowa nʼkuima pakati pawo ndipo anawauza kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 20 Atanena zimenezi, anawaonetsa manja ake ndi munthiti mwake.+ Choncho ophunzirawo anasangalala ataona Ambuyewo.+
-