55 Komanso azimayi ambiri ochokera ku Galileya amene ankatsatira Yesu kuti azimutumikira, anali komweko nʼkumaonerera chapatali.+56 Ena mwa iwo anali Mariya wa ku Magadala, Mariya mayi a Yakobo ndi Yose, ndiponso panali mayi a Yakobo ndi Yohane.*+
40 Panalinso azimayi amene ankaonerera chapatali ndithu. Ena mwa iwo anali Mariya wa ku Magadala, Mariya mayi a Yakobo Wamngʼono ndi Yose komanso panali Salome,+