Yohane 13:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Mmodzi wa ophunzirawo, amene Yesu ankamukonda,+ anakhala pafupi ndi Yesu.* Yohane 21:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Zitatero, wophunzira amene Yesu ankamukonda kwambiri uja+ anauza Petulo kuti: “Ndi Ambuye!” Simoni Petulo atamva kuti ndi Ambuye, anavala malaya ake akunja, chifukwa anali maliseche,* ndipo analumphira mʼnyanja. Yohane 21:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Petulo anatembenuka nʼkuona wophunzira amene Yesu ankamukonda uja+ akuwatsatira. Wophunzira ameneyu ndi amene pa chakudya chamadzulo chija anatsamira pachifuwa cha Yesu nʼkumufunsa kuti: “Ambuye, ndi ndani amene akufuna kukuperekani?”
7 Zitatero, wophunzira amene Yesu ankamukonda kwambiri uja+ anauza Petulo kuti: “Ndi Ambuye!” Simoni Petulo atamva kuti ndi Ambuye, anavala malaya ake akunja, chifukwa anali maliseche,* ndipo analumphira mʼnyanja.
20 Petulo anatembenuka nʼkuona wophunzira amene Yesu ankamukonda uja+ akuwatsatira. Wophunzira ameneyu ndi amene pa chakudya chamadzulo chija anatsamira pachifuwa cha Yesu nʼkumufunsa kuti: “Ambuye, ndi ndani amene akufuna kukuperekani?”