Salimo 34:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Mngelo wa Yehova amamanga msasa kuzungulira anthu onse amene amaopa Mulungu,+Ndipo amawapulumutsa.+ Machitidwe 12:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Koma mwadzidzidzi, mngelo wa Yehova* anafika,+ ndipo mʼchipinda cha ndendeyo munawala. Kenako mngeloyo anadzutsa Petulo pomugwedeza mʼnthiti nʼkunena kuti: “Dzuka msanga!” Atatero maunyolo amene anamumanga nawo manjawo anagwa pansi.+ Machitidwe 16:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Mwadzidzidzi panachitika chivomerezi champhamvu, mpaka maziko a ndendeyo anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse zinatseguka, ndipo aliyense unyolo wake unamasuka.+ Aheberi 1:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Ndiponso ponena za angelo, iye akuti: “Amachititsa kuti angelo ake akhale amphamvu* ndipo amachititsa atumiki ake+ kukhala ngati lawi la moto.”+ Aheberi 1:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Angelo onse ndi mizimu yotumikira ena.*+ Mulungu amawatumiza kuti akatumikire omwe iye adzawapulumutse.
7 Mngelo wa Yehova amamanga msasa kuzungulira anthu onse amene amaopa Mulungu,+Ndipo amawapulumutsa.+
7 Koma mwadzidzidzi, mngelo wa Yehova* anafika,+ ndipo mʼchipinda cha ndendeyo munawala. Kenako mngeloyo anadzutsa Petulo pomugwedeza mʼnthiti nʼkunena kuti: “Dzuka msanga!” Atatero maunyolo amene anamumanga nawo manjawo anagwa pansi.+
26 Mwadzidzidzi panachitika chivomerezi champhamvu, mpaka maziko a ndendeyo anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse zinatseguka, ndipo aliyense unyolo wake unamasuka.+
7 Ndiponso ponena za angelo, iye akuti: “Amachititsa kuti angelo ake akhale amphamvu* ndipo amachititsa atumiki ake+ kukhala ngati lawi la moto.”+
14 Angelo onse ndi mizimu yotumikira ena.*+ Mulungu amawatumiza kuti akatumikire omwe iye adzawapulumutse.