2 Atafika pafupi, anazindikira kuti pachitika chivomerezi champhamvu, chifukwa mngelo wa Yehova anatsika kumwamba ndipo anafika nʼkugubuduza chimwala chija, nʼkukhala pachimwalapo.+ 3 Mngeloyo ankaoneka ngati mphezi ndipo zovala zake zinali zoyera kwambiri.+