-
Mateyu 27:5-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Choncho iye anaponya ndalama zasiliva zija mʼkachisi nʼkuchoka. Kenako anapita kukadzimangirira.+ 6 Koma ansembe aakulu anatenga ndalama zasilivazo nʼkunena kuti: “Nʼzosaloleka kuti ndalamazi ziikidwe mʼmalo opatulika osungiramo chuma, chifukwa ndi malipiro a magazi.” 7 Atakambirana, anagwiritsa ntchito ndalamazo pogulira munda wa woumba mbiya kuti ukhale manda a alendo. 8 Choncho munda umenewu umatchedwa Munda wa Magazi+ mpaka lero.
-