2 ndipo anawafunsa kuti: “Kodi munalandira mzimu woyera mutakhala okhulupirira?”+ Iwo anamuyankha kuti: “Ifetu sitinamvepo kuti kuli mzimu woyera.” 3 Iye anawafunsanso kuti: “Nanga munabatizidwa ubatizo wamtundu wanji?” Iwo anayankha kuti: “Tinabatizidwa ubatizo wa Yohane.”+