12 Ndiyeno Hananiya, munthu woopa Mulungu mogwirizana ndi Chilamulo, amene anali ndi mbiri yabwino pakati pa Ayuda onse akumeneko, 13 anabwera. Iye anaima chapafupi nʼkunena kuti: ‘Mʼbale wanga Saulo, yambanso kuona!’ Nthawi yomweyo ndinakweza maso anga nʼkumuona.+