-
Machitidwe 11:5-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 “Ine ndikupemphera mumzinda wa Yopa, ndinaona masomphenya. Ndinaona chinthu chooneka ngati chinsalu chachikulu chikutsika kuchokera kumwamba. Chinthucho anachigwira mʼmakona onse 4 nʼkuchitsitsira pamene ndinali.+ 6 Nditachiyangʼanitsitsa, ndinaonamo nyama za miyendo 4 zapadziko lapansi, nyama zakutchire, nyama zokwawa komanso mbalame zamumlengalenga. 7 Ndinamvanso mawu akuti: ‘Petulo, nyamuka ndipo uphe zinthu zimenezi nʼkudya.’ 8 Koma ine ndinati, ‘Ayi Ambuye, mʼkamwa mwanga simunalowepo chinthu chilichonse chodetsedwa ndiponso chonyansa.’ 9 Koma ndinamvanso mawu aja kachiwiri kuti: ‘Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa, usiyiretu kunena kuti nʼzodetsedwa.’ 10 Mawuwo anamvekanso kachitatu, ndipo kenako zonse zija zinatengedwa kupita kumwamba.
-