Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 11:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Koma musamadye nyama zotsatirazi zimene zimabzikula kapena zili ndi ziboda zogawanika: Ngamila, chifukwa imabzikula koma ziboda zake nʼzosagawanika. Nyama imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu.+

  • Levitiko 11:13-20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Izi ndi zamoyo zouluka zimene muyenera kuziona kuti ndi zonyansa. Sizikuyenera kudyedwa chifukwa ndi zonyansa: chiwombankhanga,+ nkhwazi, muimba wakuda,+ 14 mphamba wofiira, mtundu uliwonse wa mphamba wakuda, 15 mtundu uliwonse wa khwangwala, 16 nthiwatiwa, kadzidzi, kakowa, mtundu uliwonse wa kabawi, 17 nkhwezule, chiswankhono, mantchichi, 18 tsekwe, vuwo, muimba, 19 dokowe, mtundu uliwonse wa chimeza, sadzu ndi mleme. 20 Tizilombo tonse timene timapezeka tambiri, tamapiko ndiponso tamiyendo 4, ndi tonyansa kwa inu.

  • Levitiko 20:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Muzisiyanitsa nyama yoyera ndi yodetsedwa, mbalame yodetsedwa ndi yoyera.+ Musadziipitse ndi nyama, mbalame kapena chilichonse chokwawa padziko lapansi chimene ndanena kuti ndi chodetsedwa.+

  • Deuteronomo 14:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Musamadye chinthu chilichonse chonyansa.+

  • Deuteronomo 14:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Tizilombo tonse ta mapiko timene timapezeka tambiri nʼtodetsedwanso kwa inu. Timeneti simuyenera kudya.

  • Ezekieli 4:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Kenako ndinanena kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndiloleni ndisachite zimenezo. Kuyambira ndili mwana mpaka pano sindinadzidetsepo podya nyama yopezeka itafa kapena nyama yochita kukhadzulidwa ndi chilombo,+ ndipo mʼkamwa mwanga simunalowepo nyama yodetsedwa.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena