44 Pamene Petulo ankalankhula zimenezi, anthu onse amene ankamvetsera mawuwo analandira mzimu woyera.+ 45 Ndipo okhulupirira amene anabwera ndi Petulo aja, amenenso anali odulidwa, anadabwa kwambiri. Iwo anadabwa chifukwa mphatso yaulere ya mzimu woyera inaperekedwanso kwa anthu a mitundu ina.