Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Machitidwe 13:50
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 50 Koma Ayuda anauza zoipa amayi otchuka oopa Mulungu komanso amuna olemekezeka amumzindawo. Choncho iwo anachititsa kuti Paulo ndi Baranaba ayambe kuzunzidwa+ ndipo anawaponya kunja kwa mzinda wawo.

  • 1 Akorinto 15:30, 31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Nʼchifukwa chiyaninso ifeyo tikuika moyo wathu pachiswe nthawi zonse?+ 31 Tsiku lililonse ndimakhala pa ngozi yoti ndikhoza kufa. Zimenezi nʼzoona ngati mmene zilili zoona kuti ndimakunyadirani chifukwa cha ubwenzi wanu ndi Khristu Yesu Ambuye wathu.

  • 2 Akorinto 11:23-26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Kapena kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankha ngati wamisala, ineyo ndiye mtumiki wa Khristu woposa iwowo. Ndachita zambiri kuposa iwowo,+ ndinamangidwa kambirimbiri,+ ndinamenyedwa kosawerengeka ndipo ndinabwererapo lokumbakumba kambirimbiri.+ 24 Maulendo 5 Ayuda anandikwapula zikwapu 40, kuchotsera chimodzi.+ 25 Katatu anandimenya ndi ndodo.+ Kamodzi anandiponya miyala.+ Ngalawa inandiswekerapo katatu.+ Kamodzi ndinakhala panyanja usiku ndi masana wonse. 26 Ndinayenda maulendo ambirimbiri, ndinakumana ndi zoopsa mʼmitsinje komanso ndinakumana ndi achifwamba pamsewu. Ndinakumananso ndi zoopsa kuchokera kwa anthu a mtundu wanga,+ anthu a mitundu ina,+ mumzinda,+ mʼchipululu, panyanja ndi pakati pa abale achinyengo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena