-
Machitidwe 14:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Ndiyeno anthu a mitundu ina komanso Ayuda pamodzi ndi olamulira awo, anakonza chiwembu kuti achitire chipongwe atumwiwo nʼkuwaponya miyala.+ 6 Koma iwo atadziwitsidwa zimenezi, anathawira mʼmizinda ya Lukaoniya, Lusitara, Debe, ndi mʼmadera ozungulira.+ 7 Kumeneko anapitiriza kulalikira uthenga wabwino.
-