-
Machitidwe 12:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Kutacha, asilikali aja anasokonezeka kwambiri posadziwa zimene zachitikira Petulo. 19 Herode anafunafuna Petulo paliponse ndipo atalephera kumupeza, anapanikiza alonda aja ndi mafunso komanso analamula kuti awatenge nʼkukawapatsa chilango.+ Kenako Herode anachoka ku Yudeya nʼkupita ku Kaisareya, komwe anakhalako kwakanthawi ndithu.
-