25 Koma atamugoneka kuti amukwapule, Paulo anafunsa mtsogoleri wa asilikali amene anaima pamenepo kuti: “Kodi malamulo amakulolani kukwapula nzika ya Roma mlandu wake usanazengedwe?”+
27 Munthu uyu anagwidwa ndi Ayuda ndipo anatsala pangʼono kumupha. Koma nthawi yomweyo ndinafika ndi gulu langa la asilikali nʼkumupulumutsa,+ chifukwa ndinamva kuti iyeyu ndi nzika ya Roma.+