-
Machitidwe 22:27-29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Zitatero mkulu wa asilikaliyo anabwera nʼkunena kuti: “Tandiuza, kodi nʼzoona kuti ndiwe nzika ya Roma?” Iye anati: “Inde.” 28 Mkulu wa asilikaliyo anati: “Ine ndinagula ufulu wokhala nzika ndi ndalama zambiri.” Paulo anati: “Koma ine wanga ndinachita kubadwa nawo.”+
29 Nthawi yomweyo amuna amene ankafuna kumufunsa mafunso, uku akumukwapula, anachoka nʼkumusiya. Nayenso mkulu wa asilikali uja anachita mantha atadziwa kuti munthu amene anamumangayo ndi nzika ya Roma.+
-