-
2 Akorinto 1:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Atamandike Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu,+ Bambo wachifundo chachikulu+ ndiponso Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse,+ 4 amenenso amatitonthoza* pa mayesero* athu onse,+ kuti tithe kutonthoza amene akukumana ndi mayesero*+ amtundu uliwonse, chifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.+
-