17 Atate amandikonda+ chifukwa chakuti ndikupereka moyo wanga+ kuti ndikaulandirenso. 18 Palibe munthu amene akuchotsa moyo wanga, koma ndikuupereka mwa kufuna kwanga. Ndili ndi mphamvu zoupereka komanso ndili ndi mphamvu zoulandiranso.+ Atate wanga ndi amene anandilamula kuti ndichite zimenezi.”