-
Aefeso 4:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Choncho ndikunena komanso kuchitira umboni mwa Ambuye, kuti musapitirize kuyenda ngati mmene anthu a mitundu ina amayendera,+ potsatira maganizo awo opanda pake.+ 18 Iwo ali mumdima wa maganizo ndipo ndi otalikirana ndi moyo umene umachokera kwa Mulungu, chifukwa cha umbuli umene uli mwa iwo komanso chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo.
-