1 Mafumu 17:21, 22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Ndiyeno anakumbatira mwanayo katatu ali pabedipo nʼkufuulira Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, chonde chititsani kuti moyo wa mwanayu ubwerere.” 22 Yehova anamva pemphero la Eliya+ ndipo moyo wa mwanayo unabwerera moti anakhalanso wamoyo.+ 2 Mafumu 4:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Elisa atalowa mʼnyumbamo, anapeza mwana wakufayo atamʼgoneka pabedi lake lija.+ 2 Mafumu 4:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Kenako anapita pabedipo ndipo anagwada nʼkuweramira mwanayo. Anagunditsa pakamwa pake ndi pakamwa pa mwanayo, maso ake ndi maso a mwanayo komanso manja ake ndi manja a mwanayo. Anakhalabe choncho mpaka thupi la mwanayo linayamba kutentha.+
21 Ndiyeno anakumbatira mwanayo katatu ali pabedipo nʼkufuulira Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, chonde chititsani kuti moyo wa mwanayu ubwerere.” 22 Yehova anamva pemphero la Eliya+ ndipo moyo wa mwanayo unabwerera moti anakhalanso wamoyo.+
34 Kenako anapita pabedipo ndipo anagwada nʼkuweramira mwanayo. Anagunditsa pakamwa pake ndi pakamwa pa mwanayo, maso ake ndi maso a mwanayo komanso manja ake ndi manja a mwanayo. Anakhalabe choncho mpaka thupi la mwanayo linayamba kutentha.+