-
Machitidwe 19:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Koma ena anapitiriza kuchita makani komanso sankakhulupirira, ndipo ankanena zonyoza Njirayo+ pamaso pa anthu ambiri. Choncho iye anawachokera+ nʼkuchotsanso ophunzirawo pakati pawo. Ndipo tsiku ndi tsiku ankakamba nkhani muholo pasukulu ya Turano. 10 Izi zinachitika kwa zaka ziwiri, moti anthu onse okhala mʼchigawo cha Asia, Ayuda ndi Agiriki omwe, anamva mawu a Ambuye.
-