“Dzina la Mulungu litamandike mpaka kalekale,
Chifukwa nzeru ndi mphamvu ndi zake.+
21 Iye amasintha nthawi ndi nyengo,+
Amachotsa mafumu komanso kuika mafumu,+
Amapereka nzeru kwa anthu anzeru ndiponso amachititsa kuti anthu ozindikira adziwe zinthu.+