-
Chivumbulutso 1:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Komanso kuchokera kwa Yesu Khristu, “Mboni Yokhulupirika,”+ “woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa”+ ndiponso “Wolamulira mafumu a dziko lapansi.”+
Kwa iye amene amatikonda+ komanso amene anatimasula ku machimo athu pogwiritsa ntchito magazi ake,+ 6 nʼkutipanga kukhala mafumu+ ndi ansembe+ kuti titumikire Mulungu wake ndi Atate wake, kwa iyeyo kukhale ulemerero ndi mphamvu kwamuyaya. Ame.
-