-
Luka 10:26-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi mʼChilamulo analembamo chiyani? Umawerengamo zotani?” 27 Iye anayankha kuti: “‘Muzikonda Yehova* Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, mphamvu zanu zonse ndi maganizo anu onse.’+ Komanso ‘uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”+ 28 Yesu anamuuza kuti: “Wayankha molondola. Uzichita zimenezo ndipo udzapeza moyo.”+
-