-
Agalatiya 4:4-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Koma nthawi itakwana, Mulungu anatumiza Mwana wake, amene anabadwa kudzera mwa mkazi+ ndipo anakhala pansi pa chilamulo.+ 5 Anachita zimenezi kuti apereke malipiro omasulira anthu amene anali pansi pa chilamulo+ nʼcholinga choti Mulungu atitenge nʼkukhala ana ake.+
6 Tsopano popeza ndinu ana ake, Mulunguyo watumiza mzimu+ wa Mwana wake mʼmitima yathu+ ndipo mzimuwo ukufuula kuti: “Abba,* Atate!”+
-