38 Tsopano dziwani abale anga kuti, ife tikulalikira kwa inu za kukhululukidwa kwa machimo kudzera mwa ameneyu.+ 39 Dziwaninso kuti pa zinthu zonse zimene kunali kosatheka kuti muonedwe opanda mlandu kudzera mʼChilamulo cha Mose,+ aliyense wokhulupirira akuonedwa wopanda mlandu kudzera mwa iyeyu.+