-
Luka 22:24-26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Kenako anayamba kukangana kwambiri za amene anali wamkulu kwambiri.+ 25 Koma Yesu anawauza kuti: “Mafumu a anthu a mitundu ina amachita ulamuliro pa anthu awo, ndipo amene ali ndi mphamvu pa anthuwo amadziwika kuti ndi anthu amene amachitira ena zabwino.+ 26 Inu musakhale otero.+ Koma amene ali wamkulu kwambiri pa nonsenu akhale ngati wamngʼono+ kwambiri pa nonsenu, ndipo amene ali mtsogoleri akhale ngati wotumikira.
-