-
Aroma 1:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Ine sindichita manyazi ndi uthenga wabwino.+ Kunena zoona, uthengawo ndi njira yamphamvu imene Mulungu akuigwiritsa ntchito pofuna kupulumutsa aliyense amene ali ndi chikhulupiriro,+ choyamba Ayuda+ kenako Agiriki.+ 17 Mu uthenga wabwinowu, Mulungu amaulula chilungamo chake kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro.+ Zikatero, chikhulupiriro cha anthuwo chimalimba mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Koma wolungama adzakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro chake.”+
-