-
Deuteronomo 21:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 ndipo aziuza akulu amzindawo kuti, ‘Mwana wathuyu ndi wosamva komanso ndi wopanduka ndipo amakana kutimvera. Ndi wosusuka+ komanso ndi chidakwa.’+ 21 Kenako amuna onse a mumzinda wawo azimuponya miyala nʼkumupha. Choncho muzichotsa woipayo pakati panu, ndipo Aisiraeli onse adzamva nʼkuchita mantha.+
-
-
Miyambo 23:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Usakhale mʼgulu la anthu amene amamwa vinyo wambiri.+
Usakhale mʼgulu la anthu amene amadya nyama mosusuka,+
-
1 Petulo 4:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Mʼmbuyomu munkangokhalira kuchita zofuna za anthu amʼdzikoli.+ Pa nthawi imeneyo munkachita khalidwe lopanda manyazi,* munkalakalaka zoipa, munkamwa vinyo mopitirira muyezo, munkakonda maphwando oipa,* munkapanga mipikisano yomwa mowa komanso munkapembedza mafano, komwe kunali kuphwanya malamulo.+
-
-
-