11 Ngati mzimu wa amene anaukitsa Yesu uli ndi inu, iye amene anaukitsa Khristu Yesu adzachititsanso matupi anu omwe angathe kufawo+ kukhala ndi moyo,+ pogwiritsa ntchito mzimu wake umene uli ndi inu.
19 ndi kutinso mudziwe kukula kwa mphamvu zake zopambana zimene wazisonyeza kwa okhulupirirafe.+ Mphamvu zake zazikuluzo zikuonekera muntchito zake, 20 pamene anazigwiritsa ntchito poukitsa Khristu kwa akufa nʼkumukhazika kudzanja lake lamanja+ mʼmalo akumwamba.