-
Yohane 8:36Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
36 Choncho ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.
-
-
Filimoni 15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Mwina nʼchifukwa chake anachoka kumeneko kwa nthawi yochepa,* kuti udzakhale nayenso kwamuyaya. 16 Sukhala nayenso monga kapolo,+ koma akhalanso mʼbale wokondedwa,+ amene ine ndimamukonda kwambiri. Koma iweyo uyenera kumukonda koposa pamenepo chifukwa ndi kapolo wako komanso mʼbale wako mwa Ambuye.
-