6 Koma mboni ina inanena penapake kuti: “Munthu ndi ndani kuti muzimuganizira, kapena mwana wa munthu ndi ndani kuti muzimusamalira?+ 7 Munamutsitsa pangʼono poyerekeza ndi angelo. Munamuveka ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu ndipo munamuika kuti azilamulira ntchito za manja anu.