7 Zimenezi zikukuchitikirani kuti chikhulupiriro chanu chidzachititse kuti mutamandidwe ndiponso kulandira ulemerero ndi ulemu, Yesu Khristu akadzaonekera.+ Chikhulupiriro chanucho chayesedwa+ ndipo ndi chamtengo wapatali kuposa golide amene amawonongekabe ngakhale kuti anadutsa pamoto.