Ekisodo 22:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Musamazengereze kundipatsa nsembe kuchokera pa zokolola zanu zomwe ndi zambiri komanso kuchokera ku vinyo ndi mafuta omwe ndi ochuluka.+ Mwana wanu wamwamuna woyamba kubadwa muzimupereka kwa ine.+ Miyambo 11:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Munthu wopereka mowolowa manja zinthu zidzamuyendera bwino,*+Ndipo amene amatsitsimula ena* nayenso adzatsitsimulidwa.+ Machitidwe 20:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Pa zinthu zonse ndakusonyezani kuti pogwira ntchito molimbikira chonchi,+ muzithandiza ofooka ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Paja iye anati, ‘Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri+ kuposa kulandira.’” Aheberi 13:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Komanso musaiwale kuchita zabwino ndi kugawira ena zomwe muli nazo,+ chifukwa Mulungu amasangalala ndi nsembe zoterozo.+
29 Musamazengereze kundipatsa nsembe kuchokera pa zokolola zanu zomwe ndi zambiri komanso kuchokera ku vinyo ndi mafuta omwe ndi ochuluka.+ Mwana wanu wamwamuna woyamba kubadwa muzimupereka kwa ine.+
25 Munthu wopereka mowolowa manja zinthu zidzamuyendera bwino,*+Ndipo amene amatsitsimula ena* nayenso adzatsitsimulidwa.+
35 Pa zinthu zonse ndakusonyezani kuti pogwira ntchito molimbikira chonchi,+ muzithandiza ofooka ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Paja iye anati, ‘Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri+ kuposa kulandira.’”
16 Komanso musaiwale kuchita zabwino ndi kugawira ena zomwe muli nazo,+ chifukwa Mulungu amasangalala ndi nsembe zoterozo.+