43 Limakwiriridwa lili lonyozeka, koma limaukitsidwa lili laulemerero.+ Limakwiriridwa lili lofooka, koma limaukitsidwa lili lamphamvu.+ 44 Limakwiriridwa lili thupi la mnofu, koma limaukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi la mnofu, palinso lauzimu.