-
Afilipi 3:4-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 ngakhale kuti ineyo, kuposa wina aliyense, ndili ndi zifukwa zodalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika.
Ngati pali munthu wina amene akuganiza kuti ali ndi zifukwa zodalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika, ine ndikuposa ameneyo, chifukwa: 5 ndinadulidwa pa tsiku la 8,+ ndine wa mtundu wa Isiraeli, wa fuko la Benjamini, ndine Mheberi wobadwa kwa Aheberi.+ Kunena za chilamulo, ndine Mfarisi.+ 6 Kunena za kudzipereka, ndinkazunza mpingo.+ Kunena zochita chilungamo potsatira chilamulo, ndinasonyeza kuti ndilibe chifukwa chondinenezera.
-