-
Deuteronomo 21:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 ndipo aziuza akulu amzindawo kuti, ‘Mwana wathuyu ndi wosamva komanso ndi wopanduka ndipo amakana kutimvera. Ndi wosusuka+ komanso ndi chidakwa.’+ 21 Kenako amuna onse a mumzinda wawo azimuponya miyala nʼkumupha. Choncho muzichotsa woipayo pakati panu, ndipo Aisiraeli onse adzamva nʼkuchita mantha.+
-