32 Muzipewa kukhumudwitsa Ayuda, Agiriki ndiponso mpingo wa Mulungu.+ 33 Zimenezi ndi zimene inenso ndikuyesetsa kuchita. Ndikuyesetsa kusangalatsa anthu onse pa zonse zimene ndikuchita. Sindikufuna zopindulitsa ine ndekha,+ koma zopindulitsa anthu ambiri kuti apulumutsidwe.+